10. Cikopa canga ciri ndi Mulungu, Wopulumutsa oongoka mtima.
11. Mulungu ndiye Woweruza walungama,Ndiye Mulungu wakukwiya masiku onse.
12. Akapanda kutembenuka munthu, Iye adzanola lupanga lace;Wakoka uta wace, naupiringidza.
13. Ndipo anamkonzera zida za imfa;Mibvi yace aipanga ikhale yansakali,
14. Taonani, ali m'cikuta ca zopanda pace;Anaima ndi cobvuta, nabala bodza.
15. Anacita dzenje, nalikumba,Nagwa m'mbuna yomwe anaikumba.
16. Cobvuta cace cidzambwerera mwini,Ndi ciwawa cace cidzamgwera pakati pamutu pace.
17. Ndidzayamika Yehova monga mwa cilungamo cace;Ndipo ndidzayimbira Yehova Wam'mwambamwamba.