5. Mulungu, mudziwa kupusa kwanga;Ndipo kutsutsika kwanga sikubisikira Inu.
6. Iwo akuyembekeza Inu, Ambuve Yehova wa makamu, asacite manyazi cifukwa ca ine:Iwo ofuna Inu, Mulungu wa Israyeli, asapepulidwe cifukwa ca ine.
7. Pakuti ndalola cotonza cifukwa ca Inu:Cimpepulo cakuta nkhope yanga,
8. Abale anga andiyesa mlendo,Ndi ana a mai wanga andiyesa wa mtundu wina.
9. Pakuti cangu ca pa nyumba yanu candidya;Ndi zotonza za iwo otonza Inu zandigwera ine.
10. Ndipo ndinalira pa kusala kwa moyo wanga,Koma uku kunandikhalira cotonza.
11. Ndipo cobvala canga ndinayesa ciguduli,Koma amandiphera mwambi.