29. Koma ine ndine wozunzika ndi womva zowawa;Cipulumutso canu, Mulungu, cindikweze pamsanje.
30. Ndidzalemekeza dzina la Mulungu ndi kuliyimbira,Ndipo ndidzambukitsa ndi kumyamika.
31. Ndipo cidzakomera Yehova koposa ng'ombe,Inde mphongo za nyanga ndi ziboda,
32. Ofatsa anaciona, nakondwera:Ndipo inu, ofuna Mulungu, mtima wanu ukhale ndi moyo.
33. Pakuti Yehova amvera aumphawi,Ndipo sapeputsa am'ndende ace.
34. Zakumwamba ndi dziko lapansi zimlemekeze,Nyanja ndi zonse zoyenda m'mwemo;