25. Pokhala pao pakhale bwinja;M'mahema mwao musakhale munthu.
26. Pakuti alondola amene Inu munampanda;Ndipo akambirana za zowawa zao za iwo amene munawalasa.
27. Onjezani mphulupulu pa mphulupulu zao;Ndipo asafikire cilungamo canu.
28. Afafanizidwe m'buku lamoyo,Ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama,
29. Koma ine ndine wozunzika ndi womva zowawa;Cipulumutso canu, Mulungu, cindikweze pamsanje.
30. Ndidzalemekeza dzina la Mulungu ndi kuliyimbira,Ndipo ndidzambukitsa ndi kumyamika.
31. Ndipo cidzakomera Yehova koposa ng'ombe,Inde mphongo za nyanga ndi ziboda,
32. Ofatsa anaciona, nakondwera:Ndipo inu, ofuna Mulungu, mtima wanu ukhale ndi moyo.
33. Pakuti Yehova amvera aumphawi,Ndipo sapeputsa am'ndende ace.
34. Zakumwamba ndi dziko lapansi zimlemekeze,Nyanja ndi zonse zoyenda m'mwemo;
35. Pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni, nadzamanga midzi ya Yuda;Ndipo iwo adzakhala komweko, likhale lao lao.
36. Ndipo mbumba ya atumiki ace idzalilandira;Ndipo iwo akukonda dzina lace adzakhalam'mwemo.