10. Ndipo ndinalira pa kusala kwa moyo wanga,Koma uku kunandikhalira cotonza.
11. Ndipo cobvala canga ndinayesa ciguduli,Koma amandiphera mwambi.
12. Okhala pacipata akamba za ine; Ndipo oledzera andiyimba.
13. Koma ine, pemphero langa liri kwa Inu, Yehova, m'nyengo yolandirika;Mulungu, mwa cifundo canu cacikuru,Mundibvomereze ndi coonadi ca cipulumutso canu.
14. Mundilanditse kuthope, ndisamiremo:Ndilanditseni kwa iwo akundida, ndi kwa madzi ozama.
15. Cigumula cisandifotsere,Ndipo cakuya cisandimize;Ndipo asanditsekere pakamwa pace pa dzenje.
16. Mundiyankhe Yehova; pakuti cifundo canu ncokoma;Munditembenukire monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu.
17. Ndipo musabisire nkhope yanu mtumiki wanu;Pakuti ndisautsika ine; mundiyankhe msanga.
18. Yandikizani moyo wanga, ndi kuuombola;Ndipulumutseni cifukwa ca adani anga,
19. Mudziwa cotonza canga, ndi manyazi anga, ndi cimpepulo canga:Akundisautsa ali pamaso panu,
20. Cotonza candiswera mtima, ndipo ndidwala ine;Ndipo ndinayembekeza wina wondicitira cifundo, koma palibe;Ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.
21. Ndipo anandipatsa ndulu ikhale cakudya canga;Nandimwetsa vinyo wosasa pomva ludzu ine.