1. Ndilanditseni kwa adani anga, Mulungu wanga:Ndiikeni pamsanje kwa iwo akundiukira.
2. Mundilanditse kwa ocita zopanda pace,Ndipo ndipulumutseni kwa anthu olira mwazi.
3. Pakuti onani, alalira moyo wanga;Amphamvu andipangira ciwembu:Osacimwa, osalakwa ine, Yehova,
4. Osawapatsa cifukwa ine, athamanga nadzikonza;Galamukani kukomana nane, ndipo penyani.
5. Ndinu Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israyeli,Ukani kukazonda amitundu onse:Musacitire cifundo mmodzi yense wakucita zopanda pace monyenga.
6. Abwera madzulo, auwa ngati garu,Nazungulira mudzi.
7. Onani abwetuka pakamwa pao;M'milomo mwao muli lupanga,Pakuti amati, Amva ndani?
8. Koma Inu, Yehova, mudzawaseka;Mudzalalatira amitundu onse.
9. Inu, mphamvu yanga, ndidzakulindirani;Pakuti Mulungu ndiye msanje wanga.
10. Mulungu wa cifundo canga adzandikumika:Adzandionetsa tsoka la adani anga.
11. Musawapheretu, angaiwale anthu anga:Muwabalalitse mwa mphamvu yanu, ndipo muwagwetse,Ambuye, ndinu cikopa cathu.