3. Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsaPonditonza wofuna kundimeza;Mulungu adzatumiza cifundo cace ndi coonadi cace.
4. Moyo wanga uli pakati pa mikango;Ndigona pakati pa oyaka moto,Ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mibvi,Ndipo lilime lao ndilio lupanga lakuthwa.
5. Mukwezeke m'mwambamwa mba, Mulungu;Ulemerero wanu ukhale pamwamba pa dziko lonse lapansi.
6. Anandichera ukonde apo ndiyenda;Moyo wanga wawerama:Anandikumbira mbuna patsogolo panga;Anagwa m'kati mwace iwo okha.
7. Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima;Ndidzayimba, inde, ndidzayimba zolemekeza.
8. Galamuka, ulemu wanga; galamukani cisakasa ndi zeze:Ndidzauka ndekha mamawa.
9. Ndidzakuyamikirani mwa anthu, Ambuye:Ndidzakuyimbirani mwa mitundu.
10. Pakuti cifundo canu ncacikuru kufikira m'mwamba,Ndi coonadi canu kufikira mitambo.
11. Kwezekani m'mwambamwamba, Mulungu;Ulemerero wanu ukhale pamwamba m'dziko lonse lapansi.