6. Amemezana, alalira,Achereza mapazi anga,Popeza alindira moyo wanga.
7. Kodi adzapulumuka ndi zopanda pace?Gwetsani anthu mumkwiyo, Mulungu.
8. Muwerenga kuthawathawa kwanga:Sungani misozi yanga m'nsupa yanu;Kodi siikhala m'buku mwanu?
9. Pamenepo adani anga adzabwerera m'mbuyo tsiku lakuitana ine:Ici ndidziwa, kuti Mulungu abvomerezana nane.
10. Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ace:Mwa Yehova ndidzalemekeza mau ace.
11. Pa Mulungu ndakhulupirira, sindidzaopa;Munthu adzandicitanji?
12. Zowindira Inu Mulungu, ziri pa ine:Ndidzakucitirani zoyamika.