5. Tsiku lonse atenderuza mau anga:Zolingirira zao zonse ziri pa ine kundicitira coipa.
6. Amemezana, alalira,Achereza mapazi anga,Popeza alindira moyo wanga.
7. Kodi adzapulumuka ndi zopanda pace?Gwetsani anthu mumkwiyo, Mulungu.
8. Muwerenga kuthawathawa kwanga:Sungani misozi yanga m'nsupa yanu;Kodi siikhala m'buku mwanu?
9. Pamenepo adani anga adzabwerera m'mbuyo tsiku lakuitana ine:Ici ndidziwa, kuti Mulungu abvomerezana nane.