1. Mundicitire cifundo, Mulungu, pakuti anthu afuna kundimeza:Andipsinja pondithira nkhondo tsiku lonse.
2. Adani anga afuna kundimeza tsiku lonse:Pakuti ambiri andithira nkhondo modzikuza.
3. Tsiku lakuopa ine,Ndidzakhulupirira Inu.
4. Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ace:Ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa;Anthu adzandicitanji?
5. Tsiku lonse atenderuza mau anga:Zolingirira zao zonse ziri pa ine kundicitira coipa.