9. Aonongeni, Ambuye, gawani lilime lao:Pakuti ndaona ciwawa ndi ndeu m'mudzimo.
10. Izizo ziuzungulira pa malinga ace usana ndi usiku;Ndipo m'kati mwace muli zapanda pace ndi cobvuta.
11. M'kati mwace muli kusakaza:Ciwawa ndi cinyengo sizicoka m'makwalala ace.
12. Pakuti si mdani amene ananditonzayo;Pakadatero ndikadacilola:Amene anadzikuza pa ine sindiye munthu wondida;Pakadatero ndikadambisalira:
13. Koma ameneyo ndiwe, munthu woyenerana nane,Tsamwali wanga, wodziwana nane.
14. Tinapangirana upo wokoma,Tinaperekeza khamu la anthu popita ku nyumba ya Mulungu.
15. Imfa iwagwere modzidzimutsa,Atsikire kumanda ali amoyo:Pakuti m'mokhala mwao muli zoipa pakati pao,
16. Koma ine ndidzapfuulira kwa Mulungu;Ndipo Yehova atizandipulumutsa.
17. Madzulo, m'mawa, ndi msana ndidzadandaula, ndi kubuula,Ndipo adzamva mau anga.