1. Cherani khutu pemphero langa, Mulungu;Ndipo musadzibisa pa kupemba kwanga.
2. Mveram, ndipo mundiyankhe:Ndiliralira m'kudandaula kwanga ndi kubuula;
3. Cifukwa ca mau a mdani,Cifukwa ca kundipsinja woipa;Pakuti andisenza zopanda pace,Ndipo adana nane mumkwiyo.
4. Mtima wanga uwawa m'kati mwanga;Ndipo zoopsa za imfa zandigwera.
5. Mantha ndi kunjenjemera zandidzera,Ndipo zoopsetsa zandikuta.
6. Ndipo ndinati, Ha, wina akadandipatsa mapiko onga a njiwaMwenzi nditauluka, ndi kukhaliratu.
7. Onani, ndikadathawira kutari,Ndikadagona m'cipululu.
8. Ndikadafulumira ndipulumukeKu mphepo yolimba ndi namondwe.
9. Aonongeni, Ambuye, gawani lilime lao:Pakuti ndaona ciwawa ndi ndeu m'mudzimo.
10. Izizo ziuzungulira pa malinga ace usana ndi usiku;Ndipo m'kati mwace muli zapanda pace ndi cobvuta.
11. M'kati mwace muli kusakaza:Ciwawa ndi cinyengo sizicoka m'makwalala ace.