6. Mudzaononga iwo akunena bodza:Munthu wokhetsa mwazi ndi wacinyengo, Yehova anyansidwa naye.
7. Koma ine, mwa kucuruka kwa cifundo canu ndidzalowa m'nyumba yanu:Ndidzagwada kuyang'ana Kacisi wanu woyera ndi kuopa Inu.
8. Yehova, munditsogolere m'cilungamo canu, cifukwa ca akundizondawo;Mulungamitse njira yanu pamaso panga.
9. Pakuti m'kamwa mwao mulibe mau okhazikika;M'kati mwao m'mosakaza;M'mero mwao ndi manda apululu:Lilime lao asyasyalika nalo.
10. Muwayese otsutsika Mulungu;Agwe nao uphungu wao:M'kucuruka kwa zolakwa zao muwapitikitse;Pakuti anapikisana ndi Inu.
11. Koma akondwere onse amene athawira kwa Inu,Apfuule mokondwera kosaleka, popeza muwafungatira;Nasekere mwa Inu iwo akukonda dzina lanu.
12. Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo;Mudzamcinjiriza naco cibvomerezo ngati cikopa.