5. Anapenya mudziwo, ndipo pamenepo anadabwa;Anaopsedwa, nathawako.
6. Pomwepo anagwidwa nako kunthunthumira;Anamva cowawa, ngati wam'cikuta.
7. Muswa zombo za ku Tarisi ndi mphepo ya kum'mawa.
8. Monga tidamva, momwemo tidapenyaM'mudzi wa Yehova wa makamu, m'mudzi wa Mulungu wathu:Mulungu adzaukhazikitsa ku nthawi yamuyaya.
9. Tidalingalira za cifundo canu, Mulungu,M'kati mwa Kacisi wanu.
10. Monga dzina lanu, Mulungu,Momwemo lemekezo lanu ku malekezero a dziko lapansi:M'dzanja lamanja lanu mudzala cilungamo.
11. Likondwere phiri la Ziyoni,Asekere ana akazi a Yuda,Cifukwa ca maweruzo anu.
12. Zungulirani Ziyoni, ndipo muuzinge;Werengani nsanja zace.