16. Cifukwa ca mau a wotonza wocitira mwano;Cifukwa ca mdani ndi wobwezera cilango,
17. Zonsezi zatigwera; koma sitinakuiwalani,Ndipo sitinacita monyenga m'pangano lanu.
18. Mtima wathu sunabwerera m'mbuyo,Ndipo m'mayendedwe athu sitinapatuka m'njira yanu;
19. Mungakhale munatityola mokhala zirombo,Ndi kutiphimba nao mthunzi wa imfa.
20. Tikadaiwala dzina la Mulungu wathu,Ndi kutambasulira manja athu kwa mulungu wacilendo;
21. Mulungu sakadasanthula ici kodi?Pakuti adziwa zinsinsi za mtima.
22. Koma, cifukwa ca Inu, tiphedwa tsiku lonse;Tiyesedwa ngati nkhosa zakuzipha.
23. Galamukani, mugoneranji, Ambuye?Ukani, musatitaye citayire.
24. Mubisiranji nkhope yanu,Ndi kuiwala kuzunzika ndi kupsinjika kwathu?
25. Pakuti moyo wathu waweramira kupfumbi:Pamimba pathu pakangamira dziko lapansi.
26. Ukani, tithandizeni,Tiomboleni mwa cifundo canu.