1. Colakwa ca woipayo cimati m'kati mwa mtima wanga,Palibe kuopa Mulungu pamaso pace.
2. Pakud adzidyoletsa yekha m'kuona kwace,Kuti anthu sadzacipeza coipa cace ndi kukwiya naco.
3. Mau a pakamwa pace ndiwo opanda pace ndi onyenga:Waleka kuzindikira ndi kucita bwino.
4. Alingirira zopanda pace pakama pace;Adziika panjira posad pabwino;Coipa saipidwa naco.
5. Yehova, m'mwambamuli cifundo canu;Coonadi canu cifikira kuthambo.
6. Cilungamo canu cikunga mapiri a Mulungu;Maweruzo anu akunga cozama cacikuru:Yehova, musunga munthu ndi nyama.
7. Ha! cifundo canu, Mulungu, ncokondedwadi!Ndipo ana a anthu athawira ku mthunzi wa mapiko anu.