1. Tsutsanani nao iwo akutsutsana nane, Yehova:Limbanani nao iwo akulimbana nane.
2. Gwirani cikopa cocinjiriza, Ukani kundithandiza.
3. Sololani nthungo, ndipo muwatsekerezere kunjira akundilondola:Nenani ndi moyo wanga, Cipulumutso cako ndine.
4. Athe nzeru nacite manyazi iwo akufuna moyo wanga:Abwezedwe m'mbuyo nasokonezeke iwo akundipangira ciwembu.
5. Akhale monga mungu kumphepo,Ndipo mngelo wa Yehova awapitikitse.