1. Ndakhulupirira Inu, Yehova, ndikhale wopanda manyazi nthawi zonse:Mwa cilungamo canu ndipulumutseni ine.
2. Mundicherere khutu lanu; ndipulumutseni msanga:Mundikhalire ine thanthwe lolimba, nyumba yamalinga yakundisunga.
3. Pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa;Ndipo cifukwa ca dzina lanu ndiyendetseni bwino, ndipo nditsogolereni.
4. Mundionjole m'ukonde umene anandichera mobisika.Pakuti Inu ndinu mphamvu yanga.
5. Ndipereka mzimu wanga m'dzanja lanu:Mwandiombola, Inu Yehova, Mulungu wa coonadi.
6. Ndikwiya nao iwo akusamala zacabe zonama:Koma ndikhulupirira Yehova.
7. Ndidzakondwera ndi kusangalala m'cifundo canu:Pakuti mudapenya zunzo langa;Ndipo mudadziwa mzimu wanga mu nsautso yanga:
8. Ndipo simunandipereka m'dzanja la mdani;Munapondetsa mapazi anga pali malo.
9. Mundicitire cifundo, Yehova, pakuti ndasautsika ine:Diso langa, mzimu wanga, ndi mimba yanga, zapuwala ndi mabvuto,
10. Pakuti moyo wanga watha ndi cisoni, ndi zaka zanga zatha ndi kuusa moyo:Mphamvu yanga yafoka cifukwa ca kusakaza kwanga, ndi mafupa anga apuwala.