19. Penyani adani anga, popeza acuruka;Ndipo andida ndi udani waciwawa.
20. Sungani moyo wanga, ndilanditseni,Ndisakhale nao manyazi, pakuti ndakhulupirira Inu.
21. Ungwiro ndi kuongoka mtima zindisunge,Pakuti ndayembekezera Inu.
22. Ombolani Israyeli, Mulungu, M'masautso ace onse.