3. Koma Inu ndinu woyera,Wakukhala m'malemekezo a Israyeli.
4. Makolo athu anakhulupirira Inu:Anakhulupirira, ndipo munawalanditsa.
5. Anapfuula kwa Inu, napulumutsidwa:Anakhulupita Inu, ndipo sanacita manyazi.
6. Koma ine ndine nyongolotsi, si munthu ai:Cotonza ca anthu, ndi wonyozedwa ndi anthu.
7. Onse akundipenya andiseka:Akwenzula, apukusa mutu, nati,
8. Adadzitengera kwa Yehova; kuti adzampulumutsa,Amlanditse tsopano popeza akondwera naye.
9. Pakuti Inu ndinu wondibadwitsa:Wondikhulupiritsa pokhala ine pa bere la mai wanga.
10. Cibadwire ine anandisiyira Inu:Kuyambira kwa mai wanga Mulungu wanga ndinu.
11. Musandikhalire kutali; pakuti nsautso iri pafupi:Pakuti palibe mthandizi.
12. Ng'ombe zamphongo zambiri zandizinga:Mphongo zolimba za ku Basana zandizungulira,
13. Andiyasamira m'kamwa mwao,Ngati mkango wozomola ndi wobangula.
14. Ndathiridwa pansi monga madzi,Ndipo mafupa anga onse anaguluka:Mtima wanga ukunga sera; Wasungunuka m'kati mwa matumbo anga,
15. Mphamvu yanga yauma ngati phale;Ndi lilime langa likangamira ku nsaya zanga;Ndipo mwandifikitsa ku pfumbi la imfa.
16. Pakuti andizinga agaru:Msonkhano wa oipa wanditsekereza;Andiboola m'manja anga ndi m'mapazi anga.