9. Mudzawaika ngati ng'anjo yamoto pa nyengo ya mkwiyo wanu.Yehova adzawatha m'kukwiya kwace,Ndipo moto udzawanyeketsa.
10. Mudzaziononga zobala zao kuzicotsa pa dziko lapansi,Ndi mbeu zao mwa ana a anthu.
11. Pakuti anakupangirani coipa:Anapangana ciwembu, osakhoza kucicita.
12. Pakuti mudzawabweza m'mbuyo,Popiringidza m'nsinga zanu pankhope pao,
13. Kwezekani, Yehova, mu mphamvu yanu:Potero tidzayimba ndi kulemekeza cilimbiko canu.