4. Wokhala m'mwambayo adzaseka;Ambuye adzawanyoza.
5. Pomwepo adzalankhula nao mu mkwiyo wace,Nadzawaopsa m'ukali wace:
6. Koma Ine ndadzoza mfumu yangaPa Ziyoni, phiri langa loyera.
7. Ndidzauza za citsimikizo:Yehova ananena ndiIne, Iwe ndiwe Mwana wanga;Ine lero ndakubala.
8. Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale colowa cako,Ndi malekezero a dziko lapansi akhale ako ako.
9. Udzawatyola ndi ndodo yacitsulo;Udzawaphwanya monga mbiya yawoumba.
10. Tsono, mafumu inu, citani mwanzeru:Langikani, oweruza inu a dziko lapansi.
11. Tumikirani Yehova ndi mantha,Ndipo kondwerani ndi cinthenthe.
12. Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m'njira,Ukayaka pang'ono pokha mkwiyo wace.Odala onse akumkhulupirira Iye.