4. Zingwe za imfa zinandizinga,Ndipo mitsinje ya zopanda pace inandiopsa.
5. Zingwe za manda zinandizinga:Misampha ya imfa inandifikira ine.
6. M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova,Ndipo ndinakuwira Mulungu wanga;Mau anga anawamva m'Kacisi mwace,Ndipo mkuwo wanga wa pankhope pace unalowa m'makutu mwace.
7. Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi.Ndi maziko a mapiri ananjenjemeraNagwedezeka, pakuti anakwiya iyeyo.
8. Unakwera utsi woturuka m'mphuno mwace:Ndi moto wa m'kamwa mwace unanyeka:Nuyakitsa makara.
9. Ndipo Iye anaweramitsa thambo, natsika;Ndipo pansi pa mapazi ace panali mdima bii.