35. Ndipo mwandipatsa cikopa ca cipulumutso canu:Ndipo dzanja lamanja lanu landigwiriziza,Ndipo cifatso canu candikuza ine.
36. Mwandipondetsa patali patali,Sanaterereka mapazi anga.
37. Ndidzalondola adani anga, ndi kuwapeza:Ndipo sindidzabwerera asanathe psiti.
38. Ndidzawapyoza kuti sangakhoze kuuka:Adzagwa pansi pa mapazi anga,
39. Pakuti mwaudizingiza mphamvu m'cuuno ku nkhondoyo:Mwandigonjetsera amene andiukira.
40. Ndipo adani anga mwawalozetsa m'mbuyo kwa ine,Kuti ndipasule ondidawo.
41. Anapfuula, koma panalibewopulumutsa;Ngakhale kwa Yehova, koma sanawabvomereza.
42. Pamenepo ndinawapera ngati pfumbi la kumphepo;Ndinawakhuthula ngati matope a pabwalo.
43. Mwandipulumutsa pa zolimbana nane za anthu;Mwandiika mutu wa amitundu;Mtundu wa anthu sindinaudziwa udzanditumikira.
44. Pakumva m'khutu za ine adzandimvera:Alendo adzandigonjera monyenga.
45. Alendo adzafota,Nadzaturuka monjenjemera m'ngaka mwao.
46. Yehova ngwa moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa;Nakwezeke Mulungu wa cipulumutso canga:
47. Ndiye Mulungu amene andibwe, zerera cilango,Nandigonjetsera mitundu ya anthu.
48. Andipulumutsa kwa adani anga:Inde mundikweza pa iwo akundiukira ine:Mundikwatula kwa munthu waciwawa.
49. Cifukwa cace Yehova ndidzakuyamikani mwa amitundu,Ndipo dzina lanu ndidzaliyimbira.
50. Alanditsa mfumu yace ndi cipulumutso cacikuru:Nacitira cifundo wodzozedwa wace,Davide, ndi mbumba yace, ku nthawi zonse.