1. Haleluya.Lemekezani Yehova kocokera kumwamba;Mlemekezeni m'misanje.
2. Mlemekezeni, angelo ace onse;Mlemekezeni, makamu ace onse.
3. Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi;Mlemekezeni, nyenyezi zonse zaunikira.
4. Mlemekezeni, m'mwambamwamba,Ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo.
5. Alemekeze dzina la Yehova;Popeza analamulira, ndipo zinalengedwa.
6. Anazikhazikanso ku nthawi za nthawi;Anazipatsa cilamulo cosatumphika.
7. Lemekezani Yehova kocokera ku dziko lapansi,Zinsomba inu, ndi malo ozama onse;