8. Amene aphimba thambo ndi mitambo,Amene akonzera mvula nthaka,Amene aphukitsa msipu pamapiri.
9. Amene apatsa zoweta cakudya cao,Ana a khungubwi alikulira.
10. Mphamvu ya kavalo siimkonda:Sakondwera nayo miyendo ya munthu.
11. Yehova akondwera nao akumuopa Iye,Iwo akuyembekeza cifundo cace.
12. Yerusalemu, lemekezani Yehova;Ziyoni, lemekezani Mulungu wanu.
13. Popeza analimbitsa mipiringidzo ya zitseko zanu:Anadalitsa ana anu m'kati mwanu.
14. Ndiyeamene akhalitsamalireanu mumtendere;Akukhutitsani ndi tirigu wakuca bwino.
15. Atumiza lamulo lace ku dziko lapansi;Mau ace athamanga liwiro.
16. Apatsa cipale cofewa ngati ubweya;Awaza cisanu ngati phulusa.
17. Aponya matalala ace ngati zidutsu:Adzaima ndani pa kuzizira kwace?
18. Atumiza mau ace nazisungunula;Aombetsa mphepo yace, ayenda madzi ace.
19. Aonetsa mau ace kwa Yakobo;Malemba ace, ndi maweruzo ace kwa Israyeli.
20. Sanatero nao anthu amtundu wina;Ndipo za maweruzo ace, sanawadziwa.Haleluya.