3. Aciritsa osweka mtima,Namanga mabala ao.
4. Awerenga nyenyezi momwe ziri;Azicha maina zonsezi.
5. Ambuye wathu ndi wamkuru ndi wa mphamvu zambiri;Nzeru yace njosatha.
6. Yehova agwiriziza ofatsa;Atsitsira oipa pansi.
7. Yamikani Yehova ndi kuthira mang'ombe;Myimbireni Mulungu wathu zamlemekeza pazeze:
8. Amene aphimba thambo ndi mitambo,Amene akonzera mvula nthaka,Amene aphukitsa msipu pamapiri.
9. Amene apatsa zoweta cakudya cao,Ana a khungubwi alikulira.
10. Mphamvu ya kavalo siimkonda:Sakondwera nayo miyendo ya munthu.
11. Yehova akondwera nao akumuopa Iye,Iwo akuyembekeza cifundo cace.
12. Yerusalemu, lemekezani Yehova;Ziyoni, lemekezani Mulungu wanu.
13. Popeza analimbitsa mipiringidzo ya zitseko zanu:Anadalitsa ana anu m'kati mwanu.