1. Haleluya;Pakuti kuyimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma;Pakuti cikondwetsa ici, cilemekezo ciyenera.
2. Yehova amanga Yerusalemu;Asokolotsa otayika a Israyeli.
3. Aciritsa osweka mtima,Namanga mabala ao.
4. Awerenga nyenyezi momwe ziri;Azicha maina zonsezi.
5. Ambuye wathu ndi wamkuru ndi wa mphamvu zambiri;Nzeru yace njosatha.
6. Yehova agwiriziza ofatsa;Atsitsira oipa pansi.
7. Yamikani Yehova ndi kuthira mang'ombe;Myimbireni Mulungu wathu zamlemekeza pazeze:
8. Amene aphimba thambo ndi mitambo,Amene akonzera mvula nthaka,Amene aphukitsa msipu pamapiri.
9. Amene apatsa zoweta cakudya cao,Ana a khungubwi alikulira.
10. Mphamvu ya kavalo siimkonda:Sakondwera nayo miyendo ya munthu.
11. Yehova akondwera nao akumuopa Iye,Iwo akuyembekeza cifundo cace.