3. Musamakhulupirira zinduna,Kapena mwana wa munthu, amene mulibe cipulumutso mwa iye.
4. Mpweya wace ucoka, abwerera kumka ku nthaka yace;Tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zace zitayika.
5. Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize,Ciyembekezo cace ciri pa Yehova, Mulungu wace;
6. Amene analenga zakumwamba ndi dziko lapansi,Nyanja ndi zonse ziri m'mwemo;Ndiye wakusunga coonadi kosatha:
7. Ndiye wakucitira ciweruzo osautsika;Ndiye wakupatsa anjala cakudya;Yehova amasula akaidi;
8. Yehova apenyetsa osaona;Yehova aongoletsa onse owerama;Yehova akonda olungama;
9. Yehova asunga alendo;Agwiriziza mwana wamasiye mkazi wamasiye;Koma akhotetsa njira ya oipa.
10. Yehova adzacita ufumu kosatha,Mulungu wako, Ziyoni, ku mibadwo mibadwo.Haleluya.