1. Haleluya;Ulemekeze Yehova, moyo wanga,
2. Ndidzalemekeza Yehovam'moyo mwanga;Ndidzayimbira zomlemekeza Mulungu wanga pokhala ndi moyo ine.
3. Musamakhulupirira zinduna,Kapena mwana wa munthu, amene mulibe cipulumutso mwa iye.
4. Mpweya wace ucoka, abwerera kumka ku nthaka yace;Tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zace zitayika.
5. Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize,Ciyembekezo cace ciri pa Yehova, Mulungu wace;
6. Amene analenga zakumwamba ndi dziko lapansi,Nyanja ndi zonse ziri m'mwemo;Ndiye wakusunga coonadi kosatha: