7. Adzabukitsa cikumbukilo ca ubwino wanu waukuru,Nadzayimbira cilungamo canu.
8. Yehova ndiye wacisomo, ndi wacifundo;Osakwiya msanga, ndi wa cifundo cacikuru.
9. Yehova acitira cokoma onse;Ndi nsoni zokoma zace zigwera nchito zace zonse.
10. Nchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova;Ndi okondedwa anu adzakulemekezani.
11. Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu,Adzalankhulira mphamvu yanu;
12. Kudziwitsa ana a anthu zamphamvu zace,Ndi ulemerero waukuru wa ufumu wace.
13. Ufumu wanu ndiwo ufumu womka muyaya,Ndi kuweruza kwanu kufikira mibadwo yonse yonse.
14. Yehova agwiriziza onse akugwa,Naongoletsa onse owerama.
15. Maso a onse ayembekeza Inu;Ndipo muwapatsa cakudya cao m'nyengo zao.