1. Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu;Ndipo ndidzalemekeza dzina lanu ku nthawi za nthawi.
2. Masiku onse ndidzakuyamikani;Ndi kulemekeza dzina lanu ku nthawi za nthawi.
3. Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukuru;Ndi ukulu wace ngwosasanthulika.
4. Mbadwo wina udzalemekezera nchito zanu mbadwo unzace,Ndipo udzalalikira zamphamvu zanu.
5. Ndidzalingalira ulemerero waukuru wa ulemu wanu,Ndi nchito zanu zodabwiza.