6. Angakhale Yehova ngwokwezeka, apenyanso wopepukayo;Koma wodzikuza amdziwira kutali.
7. Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo;Mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu,Ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.
8. Yehova adzanditsirizira za kwa ine:Cifundo canu, Yehova, cifikira ku nthawi zonse:Musasiye nchito za manja anu.