1. Ndikweza maso anga kwa Inu,Kwa Inu wakukhala kumwamba.
2. Taonani, monga maso a anyamata ayang'anira dzanja la ambuye ao,Monga maso a adzakazi ayang'anira dzanja la mbuye wao wamkazi:Momwemo maso athu ayang'anira Yehova Mulungu wathu,Kufikira aticitira cifundo.
3. Muticitire cifundo, Yehova, muticitire cifundo;Pakuti takhuta kwambiri ndi mnyozo.
4. Moyo wathu wakhuta ndithuNdi kuseka kwa iwo osasowa kanthu,Ndi mnyozo wa odzikuza.
Werengani mutu wathunthu Masalmo 123