1. Ndikweza maso anga kumapiri:Thandizo langa lidzera kuti?
2. Thandizo langa lidzera kwa Yehova,Wakulenga zakumwamba ndi dziko lapansi.
3. Sadzalola phazi lako literereke:Iye amene akusunga sadzaodzera.
4. Taonani, wakusunga IsrayeaSadzaodzera kapena kugona.
5. Yehova ndiye wakukusunga;Yehova ndiye mthunzi wako wa ku dzanja lako lamanja.
6. Dzuwa silidzawamba usana,Mwezi sudzakupanda usiku.
7. Yehova adzakusunga kukucotsera zoipa ziri zonse;Adzasunga moyo wako.
8. Yehova adzasungira kuturuka kwako ndi kulowa kwako,Kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.
Werengani mutu wathunthu Masalmo 121