82. Maso anga anatha mphamvu ndi kukhumba mau anu,Ndikuti, Mudzanditonthoza liti?
83. Popeza ndakhala ngati thumba lofukirira;Koma sindiiwala malemba anu.
84. Masiku a mtumiki wanu ndiwo angati?Mudzaweruza liti iwo akundilondola koipa?
85. Odzikuza anandikumbira mbuna,Ndiwo osasamalira cilamulo canu.
86. Malamulo anu onse ngokhulupirika;Andilondola nalo bodza; ndithandizeni.
87. Akadandithera pa dziko lapansi; Koma ine sindinasiya malangizo anu.
88. Mundipatse moyo monga mwa cifundo canu;Ndipo ndidzasamalira mboni ya pakamwa panu,
89. Mau anu aikika kumwamba,Kosatha, Yehova.
90. Cikhulupiriko canu cifikira mibadwo mibadwo;Munakhazikitsa dziko lapansi, ndipo likhalitsa.
91. Kunena za maweruzo anu alimbikira kufikira lero;Pakuti onsewa ndiwo atumiki anu.
92. Cilamulo canu cikadapanda kukhala cikondweretso canga,Ndikadatayika m'kuzunzika kwanga.
93. Sindidzaiwala malangizo anu nthawi zonse;Popeza munandipatsa nao moyo.
94. Ine ndine wanu, ndipulumutseniPakuti ndinafuna malangizo anu.
95. Oipa anandilalira kundiononga;Koma ndizindikira mboni zanu.
96. Ndinapenya malekezero ace a ungwiro wonse;Koma lamulo lanu ndi lotakasuka ndithu.
97. Ha! Ndikondadi cilamulo canu;Ndilingiriramo ine tsiku lonse.
98. Malamulo anu andipatsa nzeru yakuposa adani anga;Pakuti akhala nane cikhalire.