62. Pakati pa usiku ndidzauka kukuyamikaniCifukwa ca maweruzo anu olungama.
63. Ine ndine wakuyanjana nao onse akukuopani,Ndi iwo akusamalira malangizo anu.
64. Dziko lapansi lidzala naco cifundo canu, Yehova;Mundiphunzitse malemba anu.
65. Munacitira mtumiki wanu cokoma, Yehova,Monga mwa mau anu.
66. Mundiphunzitse cisiyanitso ndi nzeru;Pakuti ndinakhulupirira malamulo anu.
67. Ndisanazunzidwe ndinasokera; Koma tsopano ndisamalira mau anu.
68. Inu ndinu wabwino, ndi wakucita zabwino;Mundiphunzitse malemba anu.
69. Odzikuza anandipangira bodza:Ndidzasunga malangizo anu ndi mtima wanga wonse.
70. Mtima wao unona ngati mafuta;Koma ine ndikondwera naco cilamulo canu.
71. Kundikomera kuti ndinazunzidwa;Kuti ndiphunzire malemba anu.
72. Cilamulo ca pakamwa panu cindikomeraKoposa golidi ndi siliva zikwi zikwi.
73. Manja anu anandilenga nandiumba;Mundizindikiritse, kuti ndiphunzire malemba anu.
74. Iwo amene akuopani adzandiona ine nadzakondwera;Popeza ndayembekezera mau anu;