40. Taonani, ndinalira malangizo anu;Mundipatse moyo mwa cilungamo canu.
41. Ndipo cifundo canu cindidzere, Yehova,Ndi cipulumutso canu, monga mwa mau anu.
42. Kuti ndikhale nao mau akuyankha wonditonza;Popeza ndikhulupirira mau anu.
43. Ndipo musandicotsere ndithu mau a coonadi pakamwa panga;Pakuti ndinayembekeza maweruzo anu.
44. Potero ndidzasamalira malamulo anu cisamalireKu nthawi za nthawi.
45. Ndipo ndidzayenda mwaufulu;Popeza ndinafuna malangizo anu.
46. Ndidzalankhulanso za umboni wanu pamaso pa mafumu,Osacitapo manyazi.