153. Penyani kuzunzika kwanga, nimundilanditse;Pakuti sindiiwala cilamulo canu.
154. Mundinenere mlandu wanga, nimundiombole;Mundipatse moyo monga mwa mau anu.
155. Cipulumutso citalikira oipa;Popeza safuna malemba anu.
156. Zacifundo zanu ndi zazikuru, Yehova;Mundipatse moyo monga mwa maweruzo anu.
157. Ondilondola ndi ondisautsa ndiwoambiri;Koma sindinapatukana nazo mboni zanu.
158. Ndinapenya ocita monyenga, ndipo ndinanyansidwa nao;Popeza sasamalira mau anu.
159. Penyani kuti ndikonda malangizo anu;Mundipatse moyo, Yehova, monga mwa cifundo canu.