145. Ndinaitana ndi mtima wanga wonse; mundiyankhe, Yehova;Ndidzasunga malemba anu.
146. Ndinaitanira Inu; ndipulumutseni,Ndipo ndidzasamalira mboni zanu.
147. Ndinapfuula kusanace:Ndinayembekezera mau anu.
148. Maso anga anakumika malonda a usiku,Kuti ndilingirire mau anu.
149. Imvani liu langa monga mwa cifundo canu;Mundipatse moyo monga mwa kuweruza kwanu, Yehova.
150. Otsata zaciwembu andiyandikira;Akhala kutali ndi cilamulo canu.
151. Inu muli pafupi, Yehova;Ndipo malamulo anu onse ndiwo coonadi,
152. Kuyambira kale ndinadziwa mu mboni zanu,Kuti munazikhazika kosatha,
153. Penyani kuzunzika kwanga, nimundilanditse;Pakuti sindiiwala cilamulo canu.
154. Mundinenere mlandu wanga, nimundiombole;Mundipatse moyo monga mwa mau anu.
155. Cipulumutso citalikira oipa;Popeza safuna malemba anu.
156. Zacifundo zanu ndi zazikuru, Yehova;Mundipatse moyo monga mwa maweruzo anu.