141. Wamng'ono ine, ndi wopepulidwa;Koma sindiiwala malemba anu.
142. Cilungamo canu ndico cilungamo cosatha;Ndi cilamulo canu ndico coonadi.
143. Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera;Koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine.
144. Mboni zanu ndizo zolungama kosatha;Mundizindikiritse izi, ndipo ndidzakhala ndi moyo.
145. Ndinaitana ndi mtima wanga wonse; mundiyankhe, Yehova;Ndidzasunga malemba anu.
146. Ndinaitanira Inu; ndipulumutseni,Ndipo ndidzasamalira mboni zanu.
147. Ndinapfuula kusanace:Ndinayembekezera mau anu.
148. Maso anga anakumika malonda a usiku,Kuti ndilingirire mau anu.
149. Imvani liu langa monga mwa cifundo canu;Mundipatse moyo monga mwa kuweruza kwanu, Yehova.