109. Moyo wanga ukhala m'dzanja langa cikhalire;Koma sindiiwala cilamulo canu.
110. Oipa anandichera msampha;Koma sindinasokera m'malangizo anu.
111. Ndinalandira mboni zanu zikhale colandira cosatha;Pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga.
112. Ndinalingitsa mtima wanga ucite malemba anu,Kosatha, kufikira cimatiziro.
113. Ndidana nao a mitima iwiri;Koma ndikonda cilamulo canu.
114. Inu ndinu pobisalapo panga, ndi cikopa canga;Ndiyembekezera mau anu.
115. Mundicokere ocita zoipa inu;Kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga.