107. Ndazunzika kwambiri:Ndipatseni moyo, Yehova, monga mwa mau anu.
108. Landirani, Yehova, zopereka zaufulu za pakamwa panga,Ndipo ndiphunzitseni maweruzo anu.
109. Moyo wanga ukhala m'dzanja langa cikhalire;Koma sindiiwala cilamulo canu.
110. Oipa anandichera msampha;Koma sindinasokera m'malangizo anu.
111. Ndinalandira mboni zanu zikhale colandira cosatha;Pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga.
112. Ndinalingitsa mtima wanga ucite malemba anu,Kosatha, kufikira cimatiziro.