10. Ndinakufunani ndi mtima wanga wonse;Ndisasokere kusiyana nao malamulo anu.
11. Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga,Kuti ndisalakwire Inu.
12. Inu ndinu wodala Yehova;Ndiphunzitseni malemba anu.
13. Ndinafotokozera ndi milomo yangaMaweruzo onse a pakamwa panu,
14. Ndinakondwera m'njira ya mboni zanu,Koposa ndi cuma conse,
15. Ndidzalingirira pa malangizo anu,Ndi kupenyerera mayendedwe anu.
16. Ndidzadzikondweretsa nao malemba anu;Sindidzaiwala mau anu,
17. Mucitire cokoma mtumiki wanu kuti ndikhale ndi moyo;Ndipo ndidzasamalira mau anu.
18. Munditsegulire maso, kuti ndipenyeZodabwiza za m'cilamulo canu.
19. Ine ndine mlendo pa dziko lapansi;Musandibisire malamulo anu.
20. Mtima wanga wasweka ndi kukhumbaMaweruzo anu nyengo zonse.
21. Munadzudzula odzikuza otembereredwa,Iwo akusokera kusiyana nao malamulo anu.