1. Haleluya;Lemekezani, inu atumiki a Yehova;Lemekezani dzina la Yehova,
2. Lodala dzina la Yehova.Kuyambira tsopano kufikira kosatha.
3. Citurukire dzuwa kufikira kulowa kwaceLilemekezedwe dzina la Yehova.
4. Yehova akwezeka pamwamba pa amitundu onse,Ulemerero wace pamwambamwamba.