6. Popeza sadzagwedezeka nthawi zonse:Wolunguna adzakumbukika ku nthawi yosatha.
7. Sadzaopa mbiri yoipa;Mtima wace ngwokhazikika, wakhulupirira Yehova.
8. Mtima wace ngwocirikizika, sadzacita mantha,Kufikira ataona cofuna iye pa iwo omsautsa.
9. Anagawagawa, anapatsa aumphawi;Cilungamo cace cikhalitsa kosatha;Nyanga yace idzakwezeka ndi ulemu.
10. Woipa adzaziona, nadzapsa mtima;Adzakukuta mano, nadzasungunuka;Cokhumba oipa cidzatayika.