1. Haleluya.Wodala munthu wakuopa Yehova,Wakukondwera kwambiri ndi malamulo ace,
2. Mbeu yace idzakhala yamphamvu pa dziko lapansi;Mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa.
3. M'nyumba mwace mudzakhala akatundu ndi cuma:Ndi cilungamo cace cikhala cikhalire.
4. Kuupika kuturukira oongoka mtima mumdima;Iye ndiye wacisomo; ndi wansoni ndi wolungama.
5. Wodala munthu wakudtira cifundo, nakongoletsa;Adzalimbika nao mlandu wace poweruzidwa.
6. Popeza sadzagwedezeka nthawi zonse:Wolunguna adzakumbukika ku nthawi yosatha.