5. Yehova ayesa wolungama mtima:Koma moyo wace umuda woipa ndi iye wakukonda ciwawa.
6. Adzagwetsa pwata pwata misampha pa oipa;Moto ndi miyala yasuifure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'cikho cao.
7. Pakuti Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama:Woongoka mtima adzapenya nkhope yace.