4. Pakuti cifundo canu ncacikuru kupitirira kumwamba,Ndi coonadi canu kufikira mitambo.
5. Kwezekani pamwamba pa thambo, Mulungu;Ndi ulemerero wanu pamwamba pa dziko lonse lapansi.
6. Kuti okondedwa anu alanditsidwe,Pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja ndipo mutibvomereze.
7. Mulungu analankhula m'ciyero cace; ndidzakondwerera:Ndidzagawa Sekemu; ndidzayesa muyeso cigwa ca Sukoti.
8. Gileadi ndi wanga: Manase ndi wanga;Ndi Efraimu ndiye mphamvu ya mutu wanga;Yuda ndiye wolamulira wanga.
9. Moabu ndiye mkhate wanga;Pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga;Ndidzapfuulira Filistiya,
10. Adzandifikitsa ndani m'mudzi wa m'linga?Adzanditsogolera ndani ku Edomu?
11. Si ndinu Mulungu, amene mwatitayaOsaturuka nao magulu athu?
12. Tithandizeni mumsauko;Pakuti cipulumutso ca munthu ndi cabe.
13. Mwa Mulungu tidzacita molimbika mtima:Ndipo Iye adzapondereza otisautsa.