1. Wakhazikika mtima wanga, Mulungu;Ndidzayimba, inde ndidzayimba zolemekeza, ndiko ulemerero wanga.
2. Galamukani, cisakasa ndi zeze;Ndidzauka ndekha mamawa.
3. Ndidzakuyamikani mwa mitundu ya anthu, Yehova:Ndipo ndidzayimba zakukulemekezani mwa anthu.
4. Pakuti cifundo canu ncacikuru kupitirira kumwamba,Ndi coonadi canu kufikira mitambo.
5. Kwezekani pamwamba pa thambo, Mulungu;Ndi ulemerero wanu pamwamba pa dziko lonse lapansi.
6. Kuti okondedwa anu alanditsidwe,Pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja ndipo mutibvomereze.
7. Mulungu analankhula m'ciyero cace; ndidzakondwerera:Ndidzagawa Sekemu; ndidzayesa muyeso cigwa ca Sukoti.